Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Mateyu 22:43, 44
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 43 Iye anawafunsanso kuti: “Nanga nʼchifukwa chiyani mouziridwa ndi mzimu,+ Davide anamutchula kuti Ambuye, pamene ananena kuti, 44 ‘Yehova* anauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja mpaka nditaika adani ako pansi pa mapazi ako”’?+

  • Maliko 12:36
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 36 Kudzera mwa mzimu woyera,+ Davideyo ananena kuti, ‘Yehova* anauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja mpaka nditaika adani ako pansi pa mapazi ako.”’+

  • Luka 20:42, 43
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 42 Chifukwa Davideyo ananena mʼbuku la Masalimo kuti, ‘Yehova* anauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja 43 mpaka nditaika adani ako kuti akhale chopondapo mapazi ako.”’+

  • Machitidwe 2:34, 35
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 34 Ndipotu Davide sanapite kumwamba, koma iyeyo anati, ‘Yehova* anauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja 35 mpaka nditaika adani ako kuti akhale chopondapo mapazi ako.”’+

  • 1 Akorinto 15:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Chifukwa ayenera kukhala mfumu nʼkumalamulira mpaka Mulungu ataika adani onse pansi pa mapazi ake.+

  • Aheberi 1:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Iye amasonyeza bwino ulemerero wa Mulungu+ ndipo ndi chithunzi chenicheni cha Mulunguyo.+ Komanso mawu ake amphamvu amathandiza kuti zinthu zikhalepobe. Ndipo atatiyeretsa potichotsera machimo athu,+ anakhala kudzanja lamanja la Wolemekezeka kumwamba.+

  • Aheberi 1:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Koma kodi ndi mngelo uti amene anamuuzapo kuti: “Khala kudzanja langa lamanja, mpaka nditaika adani ako kuti akhale chopondapo mapazi ako”?+

  • Aheberi 10:12, 13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Koma munthu ameneyu anapereka nsembe imodzi yamachimo yothandiza mpaka kalekale, ndipo anakhala kudzanja lamanja la Mulungu.+ 13 Kuyambira nthawi imeneyo, akudikira mpaka pamene adani ake adzaikidwe kuti akhale chopondapo mapazi ake.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena