-
Aheberi 5:5, 6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Zilinso chimodzimodzi ndi Khristu. Iye sanadzipatse yekha ulemerero+ podziika yekha kukhala mkulu wa ansembe. Koma amene anamupatsa ulemerero umenewo ndi amene anamuuza kuti: “Iwe ndiwe mwana wanga. Lero ine ndakhala bambo ako.”+ 6 Ngatinso mmene akunenera penapake kuti: “Iwe ndiwe wansembe mpaka kalekale, mofanana ndi unsembe wa Melekizedeki.”+
-
-
Aheberi 6:19, 20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Chiyembekezo chathuchi+ chili ngati nangula* wa miyoyo yathu ndipo nʼchotsimikizika komanso chokhazikika. Chiyembekezochi chimatilowetsa mkati, kuseri kwa katani yotchingira+ 20 kumene Yesu, yemwe ndi kalambulabwalo, anakalowa chifukwa cha ife.+ Iyeyu ndi mkulu wa ansembe mpaka kalekale mofanana ndi unsembe wa Melekizedeki.+
-
-
Aheberi 7:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Kukhala ndi ansembe a fuko la Levi kunali mbali ya Chilamulo cha Mose chimene Aisiraeli anapatsidwa. Ndiye zikanakhala kuti ansembe a fuko la Levi angathandize anthu kukhala angwiro,+ kodi pakanafunikanso wansembe ngati Melekizedeki?+ Kodi sizikanakhala zokwanira kungokhala ndi wansembe ngati Aroni?
-