-
1 Samueli 1:10, 11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Hana anali wokhumudwa kwambiri ndipo anayamba kupemphera kwa Yehova+ uku akulira kwambiri. 11 Iye analonjeza kuti: “Inu Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, mukaona kuvutika kwa ine kapolo wanu nʼkundikumbukira ndiponso mukapanda kundiiwala ine kapolo wanu nʼkundipatsa mwana wamwamuna,+ ndidzamʼpereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake ndipo lezala silidzadutsa mʼmutu mwake.”+
-
-
2 Samueli 16:11, 12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Kenako Davide anauza Abisai ndi atumiki ake onse kuti: “Ngati mwana wanga weniweni, wobereka ndekha akufunafuna moyo wanga,+ kuli bwanji munthu wa fuko la Benjaminiyu?+ Musiyeni anyoze, chifukwa Yehova ndi amene wamuuza. 12 Mwina Yehova aona mavuto anga,+ ndipo Yehova adzabwezeretsa zabwino kwa ine mʼmalo mwa zimene Simeyi akunena lero pondinyoza.”+
-
-
Yesaya 38:9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Hezekiya mfumu ya Yuda atadwala nʼkuchira, analemba zotsatirazi.
-