1 Mbiri 21:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Davide atamva zimenezo, anauza Gadi kuti: “Zimenezi zikundisowetsa mtendere kwambiri. Kuli bwino ndilangidwe ndi Yehova, chifukwa chifundo chake nʼchachikulu,+ koma ndisalangidwe ndi munthu.”+ Salimo 86:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Koma inu Yehova, ndinu Mulungu wachifundo komanso wokoma mtima,Wosakwiya msanga, wachikondi chokhulupirika chochuluka ndiponso wokhulupirika.*+ Yesaya 55:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Munthu woipa asiye njira yake+Ndipo wopweteka anzake asiye maganizo ake.Iye abwerere kwa Yehova ndipo adzamuchitira chifundo.+Abwerere kwa Mulungu wathu, chifukwa adzamukhululukira ndi mtima wonse.+ 2 Akorinto 1:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Atamandike Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu,+ Bambo wachifundo chachikulu+ ndiponso Mulungu amene amatitonthoza pa vuto lililonse,+ Yakobo 5:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Monga mmene mukudziwira, anthu amene anapirira timawaona kuti ndi odala.*+ Munamva za kupirira kwa Yobu+ ndipo mukudziwa madalitso amene Yehova* anamupatsa.+ Mukuona nokha kuti Yehova* ndi wachikondi chachikulu komanso wachifundo.+
13 Davide atamva zimenezo, anauza Gadi kuti: “Zimenezi zikundisowetsa mtendere kwambiri. Kuli bwino ndilangidwe ndi Yehova, chifukwa chifundo chake nʼchachikulu,+ koma ndisalangidwe ndi munthu.”+
15 Koma inu Yehova, ndinu Mulungu wachifundo komanso wokoma mtima,Wosakwiya msanga, wachikondi chokhulupirika chochuluka ndiponso wokhulupirika.*+
7 Munthu woipa asiye njira yake+Ndipo wopweteka anzake asiye maganizo ake.Iye abwerere kwa Yehova ndipo adzamuchitira chifundo.+Abwerere kwa Mulungu wathu, chifukwa adzamukhululukira ndi mtima wonse.+
3 Atamandike Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu,+ Bambo wachifundo chachikulu+ ndiponso Mulungu amene amatitonthoza pa vuto lililonse,+
11 Monga mmene mukudziwira, anthu amene anapirira timawaona kuti ndi odala.*+ Munamva za kupirira kwa Yobu+ ndipo mukudziwa madalitso amene Yehova* anamupatsa.+ Mukuona nokha kuti Yehova* ndi wachikondi chachikulu komanso wachifundo.+