-
1 Mbiri 15:12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Ndiyeno anawauza kuti: “Inuyo ndinu atsogoleri a nyumba za makolo a Alevi. Choncho inu ndi abale anu mudziyeretse ndipo mukatenge Likasa la Yehova Mulungu wa Isiraeli nʼkukaliika kumalo amene ndakonza kuti lizikhalako.
-
-
Machitidwe 7:45, 46Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
45 Makolo athu analandira chihemachi kwa makolo awo ndipo analowa nacho limodzi ndi Yoswa mʼdziko limene munali anthu a mitundu ina.+ Anthu amenewa Mulungu anawathamangitsa pamaso pa makolo athu+ ndipo chihemacho chinakhala mʼdzikoli mpaka nthawi ya Davide. 46 Mulungu anakomera mtima Davide ndipo iye anapempha mwayi woti amange nyumba yoti Mulungu wa Yakobo azikhalamo.+
-