17 Koma inu Yehova mudzamva pempho la anthu ofatsa.+
Mudzalimbitsa mitima yawo+ ndipo mudzawamvetsera mwatcheru.+
18 Mudzaweruza mwachilungamo mwana wamasiye komanso anthu oponderezedwa,+
Kuti munthu wamba wochokera kufumbi asadzawachititsenso mantha.+