-
Mika 6:6-8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Kodi nditenge chiyani popita kwa Yehova?
Ndikagwade ndi chiyani kwa Mulungu wakumwamba?
Kodi ndipite nditatenga nsembe zopsereza zathunthu?
Ndiponso ana a ngʼombe achaka chimodzi?+
7 Kodi Yehova adzasangalala ndi masauzande a nkhosa zamphongo?
Kodi adzakondwera ndi mitsinje ya mafuta masauzande ambirimbiri?+
Kodi ndipereke mwana wanga wamwamuna woyamba chifukwa cha zolakwa zanga,
Ndipereke chipatso cha mimba yanga chifukwa cha tchimo langa?+
8 Iye anakuuza munthu iwe zimene zili zabwino.
Kodi Yehova akufuna kuti uzichita* chiyani?
-