-
Deuteronomo 10:12, 13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Tsopano Aisiraeli inu, kodi Yehova Mulungu wanu akufuna kuti muzichita chiyani?+ Akufuna kuti muzichita izi: muziopa Yehova Mulungu wanu,+ muziyenda mʼnjira zake zonse,+ muzikonda ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse komanso moyo wanu wonse,+ 13 ndiponso kuti muzisunga malamulo a Yehova ndi malangizo ake amene ndikukupatsani lero, kuti zinthu zikuyendereni bwino.+
-