Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 1:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Kenako Mulungu anati: “Tiyeni+ tipange munthu mʼchifaniziro+ chathu, kuti akhale wofanana nafe.+ Ayangʼanire nsomba zamʼnyanja, zamoyo zouluka mumlengalenga, nyama zoweta ndiponso nyama iliyonse yokwawa padziko lapansi. Komanso asamalire dziko lonse lapansi.”+

  • Yohane 1:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 1 Pachiyambi, panali wina amene ankadziwika kuti Mawu,+ ndipo Mawuyo anali ndi Mulungu+ komanso Mawuyo anali mulungu.*+

  • Yohane 1:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Zinthu zonse zinakhalako kudzera mwa iye+ ndipo palibe chinthu ngakhale chimodzi chimene chinakhalapo popanda iyeyo.

  • Yohane 17:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Ndiye tsopano Atate, ndiloleni kuti ndikhale pambali panu ndipo mundipatse ulemerero umene ndinali nawo pambali panu dziko lisanakhalepo.+

  • Akolose 1:15, 16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Iye ndi chifaniziro cha Mulungu wosaonekayo,+ woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse.+ 16 Kudzera mwa iye, Mulungu analenga zinthu zina zonse kumwamba ndi padziko lapansi. Analenga zinthu zooneka ndi zinthu zosaoneka,+ kaya ndi mipando yachifumu, ambuye, maboma komanso maulamuliro. Inde, analenga zinthu zina zonse kudzera mwa iye+ ndiponso chifukwa cha iye.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena