34 Ana a njoka inu,+ mungalankhule bwanji zinthu zabwino pamene muli oipa? Chifukwa pakamwa pamalankhula zosefukira mumtima.+ 35 Munthu wabwino amatulutsa zabwino mʼchuma chabwino chamumtima mwake, koma munthu woipa amatulutsa zoipa mʼchuma choipa chamumtima mwake.+