-
Mateyu 22:37-40Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
37 Iye anamuyankha kuti: “‘Muzikonda Yehova* Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse ndi maganizo anu onse.’+ 38 Limeneli ndi lamulo lalikulu kwambiri komanso loyamba. 39 Lachiwiri lofanana nalo ndi ili: ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’+ 40 Chilamulo chonse chagona pa malamulo awiri amenewa, kuphatikizaponso zimene aneneri analemba.”+
-