-
Miyambo 5:8-10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Ukhale kutali kwambiri ndi iye.
Usayandikire pakhomo la nyumba yake,+
9 Kuti usapereke ulemu wako kwa anthu ena+
Komanso kuti usakumane ndi mavuto mʼzaka zotsala za moyo wako.*+
10 Ndiponso kuti alendo asakuwonongere zinthu zako,*+
Komanso kuti zinthu zimene unazipeza movutikira zisapite kunyumba ya mlendo.
-
-
Luka 15:13, 14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Patangopita masiku owerengeka, mwana wamngʼono uja anasonkhanitsa zinthu zake zonse nʼkupita kudziko lina lakutali. Kumeneko anayamba kukhala moyo wotayilira ndipo anasakaza chuma chake chonse. 14 Atawononga chuma chake chonse, mʼdziko lonselo munagwa njala yaikulu ndipo iye anayamba kuvutika kwambiri.
-