-
Mlaliki 2:15, 16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Choncho mumtima mwanga ndinanena kuti: “Zimene zimachitikira opusa inenso zidzandichitikira.”+ Ndiye ndinapindula chiyani chifukwa chokhala wanzeru kwambiri? Choncho mumtima mwanga ndinanena kuti: “Izinso nʼzachabechabe.” 16 Chifukwa munthu wanzeru komanso munthu wopusa,+ onsewa sadzakumbukiridwa mpaka kalekale. Mʼmasiku amene akubwerawa aliyense adzaiwalika. Ndipo kodi wanzeru adzafa bwanji? Adzafa mofanana ndi wopusa.+
-