-
Ezara 1:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
1 Mʼchaka choyamba cha Koresi+ mfumu ya Perisiya, pokwaniritsa mawu a Yehova amene analankhula kudzera mwa Yeremiya,+ Yehova analimbikitsa Koresi mfumu ya Perisiya kuti alengeze mu ufumu wake wonse, zomwenso iye analemba mʼmakalata,+ kuti:
2 “Koresi mfumu ya Perisiya wanena kuti, ‘Yehova Mulungu wakumwamba wandipatsa maufumu onse apadziko lapansi.+ Iye wandituma kuti ndimumangire nyumba ku Yerusalemu+ mʼdziko la Yuda.
-
-
Danieli 10:1Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Mʼchaka chachitatu cha ulamuliro wa Mfumu Koresi+ ya Perisiya, Mulungu anamuululira nkhani inayake Danieli, amene ankadziwikanso ndi dzina lakuti Belitesazara.+ Nkhani imene anauzidwayo inali yoona ndipo inali yokhudza nkhondo yaikulu. Danieli anamvetsa nkhani imeneyi ndipo anathandizidwa kumvetsa zinthu zimene anaonazo.
-