-
Deuteronomo 31:16, 17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Tsopano Yehova anauza Mose kuti: “Iweyo watsala pangʼono kufa,* ndipo anthu awa adzakhala osakhulupirika kwa ine ndipo adzayamba kulambira milungu yachilendo imene ili mʼdziko limene akupita.+ Iwo adzandisiya+ nʼkuphwanya pangano limene ndinapangana nawo.+ 17 Pa nthawi imeneyo mkwiyo wanga udzawayakira+ ndipo ndidzawasiya+ nʼkuwabisira nkhope yanga+ mpaka atawonongedwa.+ Ndiyeno akadzakumana ndi masoka komanso mavuto ambiri adzanena kuti, ‘Masoka amenewatu akutigwera chifukwa chakuti Mulungu wathu sali pakati pathu.’+
-
-
Mika 3:4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Pa nthawiyo adzafuulira Yehova kuti awathandize,
Koma sadzawayankha.
-