36 ‘Nʼchifukwa chake mtima wanga udzalirire Mowabu ngati chitoliro,+
Mtima wanga udzalirira amuna a ku Kiri-haresi ngati chitoliro.
Chifukwa chuma chimene wapanga chidzawonongeka.
37 Mutu uliwonse wametedwa mpala,+
Ndipo ndevu zonse nʼzometa.
Mʼmanja monse ndi mochekekachekeka,+
Ndipo anthu onse amanga ziguduli mʼchiuno mwawo.+