-
Yesaya 28:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
28 Tsoka kwa chisoti* chokongola* cha zidakwa za ku Efuraimu+
Komanso maluwa ake okongola amene akufota!
Maluwawo avalidwa ndi mzinda umene uli paphiri, pamwamba pa chigwa chachonde, kumene zidakwa zoledzera ndi vinyozo zimakhala.
2 Taonani! Yehova ali ndi winawake wamphamvu komanso wanyonga.
Mofanana ndi mvula yamabingu komanso yamatalala, mvula yamphepo yowononga,
Mofanana ndi mvula yamabingu ya madzi amphamvu osefukira,
Iye adzagwetsera pansi chisoti chaulemererocho mwamphamvu.
-
-
Hoseya 5:14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Ine ndidzakhala ngati mkango wamphamvu kwa Efuraimu,
Ndiponso ngati mkango wamphamvu kwa anthu a mʼnyumba ya Yuda.
-