Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yeremiya 50:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  3 Chifukwa mtundu wina wa anthu wabwera kudzamuukira kuchokera kumpoto.+

      Mtundu umenewu wasandutsa dziko lake kukhala chinthu chochititsa mantha.

      Palibe aliyense amene akukhala mʼdzikoli.

      Anthu ndiponso ziweto zathawa.

      Zathawira kutali.”

  • Yeremiya 50:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  9 Inetu ndikuutsa gulu lalikulu la mitundu yamphamvu

      Ndi kulibweretsa kuchokera kudziko lakumpoto kuti lidzaukire Babulo.+

      Mitunduyi idzabwera ili yokonzeka kumenya nkhondo

      Ndipo Babulo adzagonjetsedwa.

      Mauta awo ndi ofanana ndi mauta a msilikali

      Amene akupha ana.+

      Iwo sabwerera asanachitepo kanthu.

  • Yeremiya 51:27, 28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 “Kwezani chizindikiro mʼdzikoli.+

      Imbani lipenga pakati pa mitundu ya anthu.

      Sankhani* mitundu ya anthu kuti ichite naye nkhondo.

      Muitanireni maufumu a ku Ararati,+ ku Mini ndi ku Asikenazi+ kuti adzamuukire.

      Muikireni wolemba anthu usilikali.

      Mubweretsereni mahatchi ambiri ngati dzombe lingʼonolingʼono.

      28 Sankhani* mitundu ya anthu kuti ichite naye nkhondo.

      Sankhani mafumu a ku Mediya,+ abwanamkubwa ake ndi achiwiri kwa olamulira awo onse

      Komanso mayiko onse amene iwo amawalamulira.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena