Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 21:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  2 Ndauzidwa masomphenya ochititsa mantha akuti:

      Mtundu wachinyengo ukuchita zachinyengo,

      Ndipo mtundu wowononga ukuwononga.

      Pita ukachite nkhondo, iwe Elamu! Kazungulire mzindawo, iwe Mediya!+

      Ndidzathetsa mavuto onse amene mzindawo unachititsa.+

  • Yeremiya 51:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 “Nolani mivi yanu.*+ Tengani zishango zozungulira.

      Yehova walimbikitsa* mafumu a Amedi kuti akamenye nkhondo,+

      Chifukwa akufuna kuwononga Babulo.

      Yehova akubwezera Babulo, akumubwezera chifukwa cha kachisi wake.

  • Yeremiya 51:27, 28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 “Kwezani chizindikiro mʼdzikoli.+

      Imbani lipenga pakati pa mitundu ya anthu.

      Sankhani* mitundu ya anthu kuti ichite naye nkhondo.

      Muitanireni maufumu a ku Ararati,+ ku Mini ndi ku Asikenazi+ kuti adzamuukire.

      Muikireni wolemba anthu usilikali.

      Mubweretsereni mahatchi ambiri ngati dzombe lingʼonolingʼono.

      28 Sankhani* mitundu ya anthu kuti ichite naye nkhondo.

      Sankhani mafumu a ku Mediya,+ abwanamkubwa ake ndi achiwiri kwa olamulira awo onse

      Komanso mayiko onse amene iwo amawalamulira.

  • Yeremiya 51:48
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 48 Kumwamba ndi dziko lapansi komanso chilichonse cha mmenemo

      Zidzafuula mosangalala poona kuti Babulo wagwa,+

      Chifukwa owononga adzabwera kwa iye kuchokera kumpoto,”+ akutero Yehova.

  • Danieli 5:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 PERESI, ufumu wanu wagawidwa ndipo waperekedwa kwa Amedi ndi Aperisiya.”+

  • Danieli 5:30
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 30 Usiku womwewo, Belisazara mfumu ya Akasidi anaphedwa.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena