Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 6:11, 12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Atatero ndinafunsa kuti: “Mpaka liti, inu Yehova?” Iye anayankha kuti:

      “Mpaka mizinda yawo itawonongedwa nʼkukhala mabwinja

      Mpaka nyumba zawo zitakhala zopanda anthu okhalamo

      Ndiponso mpaka dziko litawonongekeratu nʼkukhala bwinja.+

      12 Mpaka Yehova atathamangitsira anthu kutali+

      Ndiponso mpaka mbali yaikulu ya dzikolo itakhala bwinja.

  • Yeremiya 26:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 “Mika+ wa ku Moreseti nayenso ankanenera mʼmasiku a Mfumu Hezekiya+ ya ku Yuda. Iye ankauza anthu onse a ku Yuda kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti:

      “Ziyoni adzalimidwa ngati munda,

      Yerusalemu adzakhala mabwinja,+

      Ndipo phiri la nyumba ya Mulungu* lidzakhala ngati zitunda zamunkhalango.”’+

  • Maliro 2:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 Yehova wakhala ngati mdani.+

      Wameza Isiraeli.

      Iye wameza nsanja zonse za Isiraeli.

      Wawononga malo ake onse okhala ndi mipanda yolimba kwambiri.

      Ndipo wachititsa kuti paliponse pakhale maliro komanso kulira mumzinda wa mwana wamkazi wa Yuda.

  • Ezekieli 36:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Choncho inu mapiri a ku Isiraeli, imvani mawu a Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wauza mapiri ndi zitunda, mitsinje ndi zigwa, mabwinja a malo amene anawonongedwa+ komanso mizinda yopanda anthu imene anthu a mitundu ina amene anapulumuka anaitenga kuti ikhale yawo. Anthuwo ankakhala moizungulira ndipo ankainyoza.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena