-
Yesaya 11:11, 12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Pa tsiku limenelo Yehova adzaperekanso dzanja lake kachiwiri kuti atenge anthu ake otsala kuchokera ku Asuri,+ ku Iguputo,+ ku Patirosi,+ ku Kusi,+ ku Elamu,+ ku Sinara,* ku Hamati ndi mʼzilumba zamʼnyanja.+ 12 Iye adzakwezera chizindikiro mitundu ya anthu nʼkusonkhanitsa Aisiraeli omwe anamwazikana.+ Ndipo adzasonkhanitsa pamodzi Ayuda omwe anabalalika, kuchokera kumakona 4 a dziko lapansi.+
-