Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 26:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Ndikadzawononga njira* zanu zopezera chakudya,+ akazi 10 adzaphika mkate mu uvuni umodzi wokha, ndipo pokugawirani mkatewo, adzachita kukuyezerani+ nʼkukupatsani wochepa. Choncho mudzadya koma simudzakhuta.+

  • Deuteronomo 28:49
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 49 Yehova adzatumiza mtundu wakutali+ kuchokera kumalekezero adziko lapansi kuti udzakuukireni. Mtunduwo udzakuukirani mofulumira kwambiri ngati mmene chiwombankhanga chimagwirira nyama.+ Mtundu umenewo chilankhulo chake simudzachimva,+

  • Deuteronomo 28:51
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 51 Iwo adzadya ana a ziweto zanu ndi zipatso za nthaka yanu mpaka mutawonongedwa. Sadzakusiyirani mbewu iliyonse, vinyo watsopano kapena mafuta, mwana wa ngʼombe kapena mwana wa nkhosa mpaka atakuwonongani.+

  • Yeremiya 37:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Choncho Mfumu Zedekiya inalamula kuti Yeremiya atsekeredwe mʼBwalo la Alonda+ ndipo tsiku lililonse ankamupatsa mtanda wozungulira wa mkate.+ Mkate umenewu unkachokera kumsewu wa ophika mkate ndipo anapitiriza kumʼpatsa mkatewo mpaka mkate wonse utatha mumzindamo.+ Choncho Yeremiya anapitiriza kukhala mʼBwalo la Alonda.

  • Ezekieli 4:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Kenako anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, ine ndidzachititsa kuti chakudya chisowe* mu Yerusalemu.+ Anthu azidzadya chakudya chochita kuyeza ndipo adzachidya ali ndi nkhawa yaikulu.+ Azidzamwa madzi ochita kuyeza ali ndi mantha aakulu.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena