-
Yeremiya 41:17, 18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Iwo anakakhala kumalo ogona alendo a Chimamu pafupi ndi Betelehemu+ nʼcholinga choti apitirize ulendo wopita ku Iguputo.+ 18 Anachita zimenezi chifukwa cha Akasidi. Iwo ankaopa Akasidiwo chifukwa chakuti Isimaeli mwana wa Netaniya anapha Gedaliya mwana wa Ahikamu, amene mfumu ya Babulo inamuika kuti azilamulira mʼdzikolo.+
-