-
Yeremiya 44:12-14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Ine ndigwira anthu amene anatsala ku Yuda omwe anatsimikiza mtima kuti apite mʼdziko la Iguputo nʼkumakakhala kumeneko, moti onsewo adzafera mʼdziko la Iguputo.+ Iwo adzaphedwa ndi lupanga komanso adzafa ndi njala. Kuyambira munthu wamba ndi wolemekezeka yemwe, onse adzaphedwa ndi lupanga komanso adzafa ndi njala. Iwo adzakhala otembereredwa, chinthu chochititsa mantha, chinthu chonyozeka ndi chochititsa manyazi.+ 13 Ndidzalanga anthu onse okhala mʼdziko la Iguputo ngati mmene ndinalangira Yerusalemu. Ndidzawalanga ndi lupanga, njala ndi mliri.*+ 14 Ndipo anthu otsala a ku Yuda amene apita kukakhala mʼdziko la Iguputo sadzathawa kapena kupulumuka kuti abwerere kudziko la Yuda. Adzafunitsitsa kubwerera kuti akakhale kumeneko koma sadzabwerera kupatulapo anthu ochepa amene adzathawe.’”
-
-
Yeremiya 44:27, 28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 Ine ndine wokonzeka kuwabweretsera tsoka, osati zinthu zabwino.+ Anthu onse a ku Yuda amene ali mʼdziko la Iguputo adzafa ndi lupanga ndiponso njala mpaka atatheratu.+ 28 Anthu ochepa okha adzathawa lupanga mʼdziko la Iguputo nʼkubwerera kudziko la Yuda.+ Ndipo pa nthawiyo, anthu amene anatsala mu Yuda amene anabwera mʼdziko la Iguputo kuti azikhalamo adzadziwa kuti mawu amene akwaniritsidwa ndi a ndani, mawu anga kapena mawu awo.”’”
-