9 Yehova wanena kuti,
‘Popeza Turo anandigalukira mobwerezabwereza,+ sindidzamusinthira chigamulo changa.
Chifukwa anapereka ku Edomu gulu lonse la anthu ogwidwa ukapolo,
Ndiponso chifukwa chakuti sanakumbukire pangano la pachibale.+
10 Choncho ndidzatumiza moto pampanda wa Turo,
Ndipo udzawotcheratu nsanja zake zolimba.’+