Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 16:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  6 Ife tamva za kunyada kwa Mowabu, iye ndi wonyada kwambiri.+

      Tamva za kudzikweza kwake, kunyada kwake ndi mkwiyo wake.+

      Koma zolankhula zake zopanda pake sizidzachitika.

  • Yesaya 25:10, 11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Dzanja la Yehova lidzateteza* phiri limeneli,+

      Ndipo Mowabu adzapondedwapondedwa mʼdziko lake lomwe+

      Ngati udzu umene wapondedwapondedwa nʼkukhala mulu wa manyowa.

      11 Iye adzamenya mzindawo ndi manja ake

      Ngati mmene munthu amamenyera madzi ndi manja ake akamasambira.

      Adzathetsa kunyada kwa mzindawo+

      Poumenya mwaluso ndi manja ake.

  • Zefaniya 2:9, 10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  9 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Pali ine Mulungu wamoyo,

      Mowabu adzakhala ngati Sodomu,+

      Ndipo Amoni adzakhala ngati Gomora,+

      Malo okhala ndi zomera zoyabwa, dothi lamchere ndiponso malo abwinja mpaka kalekale.+

      Anthu anga amene adzatsale adzatenga zinthu za anthu amenewa,

      Ndipo anthu amtundu wanga amene adzatsale, adzawalanda anthuwa zinthu zawo.

      10 Anthu amenewo adzaona zimenezi chifukwa cha kunyada kwawo,+

      Chifukwa ankanyoza anthu a Yehova wa magulu ankhondo akumwamba ndipo ankadzikweza pamaso pawo.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena