5 Choncho zinamwazikana chifukwa zinalibe mʼbusa+ ndipo zinakhala chakudya cha zilombo zonse zakutchire. 6 Nkhosa zanga zinasochera mʼmapiri onse ndi mʼzitunda zonse zitalizitali. Nkhosa zanga zinabalalika padziko lonse lapansi ndipo panalibe amene ankazifufuza kapena kuziyangʼanayangʼana.