Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 28:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  7 Amenewanso asochera chifukwa cha vinyo.

      Akuyenda modzandira chifukwa cha mowa.

      Wansembe ndi mneneri asochera chifukwa cha mowa.

      Vinyo wawasokoneza,

      Ndipo akuyenda modzandira chifukwa cha mowa.

      Sakuona bwinobwino ndipo akusochera,

      Komanso akulephera kusankha zinthu mwanzeru.+

  • Yeremiya 5:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Aneneri akulosera zabodza,+

      Ndipo ansembe akugwiritsa ntchito mphamvu zawo kuti azilamulira ena.

      Anthu anga nawonso akukonda zimenezi.+

      Koma kodi mudzachita chiyani mapeto akadzafika?”

  • Yeremiya 6:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 “Chifukwa aliyense kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, akupeza phindu mwachinyengo.+

      Kuyambira mneneri mpaka wansembe, aliyense akuchita zachinyengo.+

  • Ezekieli 22:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Aneneri ako akukonza chiwembu mʼdzikoli.+ Iwo ali ngati mkango wobangula umene wagwira nyama+ ndipo akupha anthu. Akulanda anthu chuma ndi zinthu zawo zamtengo wapatali. Apangitsa kuti akazi amasiye achuluke mʼdzikolo.

  • Zefaniya 3:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Aneneri ake ndi amwano ndiponso achinyengo.+

      Ansembe ake amaipitsa zinthu zopatulika,+

      Ndipo amaphwanya malamulo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena