Yeremiya 4:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Kenako ndinanena kuti: “Mayo ine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa! Kunena zoona, mwapusitsa kwambiri anthu awa+ ndiponso Yerusalemu ponena kuti, ‘Mudzakhala pa mtendere,’+ pamene lupanga lili pakhosi pathu.”* Yeremiya 6:13, 14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 “Chifukwa aliyense kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, akupeza phindu mwachinyengo.+Kuyambira mneneri mpaka wansembe, aliyense akuchita zachinyengo.+ 14 Iwo akuyesa kuchiritsa mwachinyengo kuwonongeka kwa anthu anga* ponena kuti,‘Kuli mtendere! Kuli mtendere!’ Pamene kulibe mtendere.+ Yeremiya 8:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Iwo akuyesa kuchiritsa mwachinyengo kuwonongeka kwa mwana wamkazi* wa anthu anga ponena kuti,‘Kuli mtendere! Kuli mtendere!’ Pamene kulibe mtendere.+ Ezekieli 13:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Zonsezi zidzachitika chifukwa chakuti iwo asocheretsa anthu anga ponena kuti, “Tili pa mtendere!” koma palibe mtendere.+ Munthu akamanga khoma lachipinda losalimba, iwo akumalipaka laimu.’*+
10 Kenako ndinanena kuti: “Mayo ine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa! Kunena zoona, mwapusitsa kwambiri anthu awa+ ndiponso Yerusalemu ponena kuti, ‘Mudzakhala pa mtendere,’+ pamene lupanga lili pakhosi pathu.”*
13 “Chifukwa aliyense kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, akupeza phindu mwachinyengo.+Kuyambira mneneri mpaka wansembe, aliyense akuchita zachinyengo.+ 14 Iwo akuyesa kuchiritsa mwachinyengo kuwonongeka kwa anthu anga* ponena kuti,‘Kuli mtendere! Kuli mtendere!’ Pamene kulibe mtendere.+
11 Iwo akuyesa kuchiritsa mwachinyengo kuwonongeka kwa mwana wamkazi* wa anthu anga ponena kuti,‘Kuli mtendere! Kuli mtendere!’ Pamene kulibe mtendere.+
10 Zonsezi zidzachitika chifukwa chakuti iwo asocheretsa anthu anga ponena kuti, “Tili pa mtendere!” koma palibe mtendere.+ Munthu akamanga khoma lachipinda losalimba, iwo akumalipaka laimu.’*+