Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yeremiya 24:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Ndidzachititsa kuti anthu a mitundu yonse padziko lapansi achite mantha akadzaona tsoka limene ndidzawabweretsere.+ Anthu adzawanyoza, adzawaona kuti ndi chitsanzo cha anthu amene akumana ndi tsoka, adzawaseka komanso kuwatemberera+ kulikonse kumene ndidzawabalalitsire.+

  • Yeremiya 42:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: ‘Mofanana ndi mmene ndinasonyezera anthu okhala mu Yerusalemu+ mkwiyo ndi ukali wanga, inunso ndidzakusonyezani mkwiyo wanga ngati mutapita ku Iguputo. Mudzakhala otembereredwa, chinthu chochititsa mantha, chinthu chonyozeka+ ndi chochititsa manyazi ndipo malo ano simudzawaonanso.’

  • Maliro 5:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Nʼchifukwa chiyani mwatiiwala kwamuyaya nʼkutisiya kwa nthawi yaitali chonchi?+

  • Danieli 9:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Inu Yehova, nthawi zonse mumachita zinthu zolungama.+ Chonde, chotsani mkwiyo wanu waukulu pa Yerusalemu, phiri lanu loyera. Chifukwa cha machimo athu ndi zolakwa za makolo athu, Yerusalemu komanso anthu anu, tikunyozedwa ndi anthu onse otizungulira.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena