Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 26:38, 39
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 38 Ambiri mwa inu mudzafa mʼdziko la anthu a mitundu ina,+ ndipo dziko la adani anu lidzakumezani. 39 Anthu amene adzatsale pakati panu adzazunzika mʼmayiko a adani awo+ chifukwa cha zolakwa zanu. Iwo adzazunzika chifukwa cha zolakwa za makolo awo.+

  • 1 Mafumu 9:7-9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 ndidzachotsa Aisiraeli mʼdziko limene ndawapatsa+ ndipo nyumba imene ndaiyeretsa chifukwa cha dzina langa, ndidzaichotsa pamaso panga.+ Aisiraeli adzatonzedwa ndi kunyozedwa pakati pa mitundu yonse ya anthu.+ 8 Nyumbayi idzakhala bwinja.+ Aliyense wodutsa pafupi adzayangʼana modabwa ndipo adzaimba mluzu nʼkunena kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani Yehova anachitira zimenezi dzikoli komanso nyumbayi?’+ 9 Ndipo adzati, ‘Nʼchifukwa chakuti anasiya Yehova Mulungu wawo amene anatulutsa makolo awo mʼdziko la Iguputo ndipo anatenga milungu ina nʼkumaigwadira ndi kuitumikira. Nʼchifukwa chake Yehova anawabweretsera tsoka lonseli.’”+

  • Salimo 79:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 79 Inu Mulungu, anthu a mitundu ina alowa mʼdziko limene ndi cholowa chanu.+

      Aipitsa kachisi wanu woyera.+

      Yerusalemu amusandutsa bwinja.+

  • Salimo 79:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Anthu oyandikana nafe akutinyoza,+

      Anthu otizungulira akutiseka komanso kutikuwiza.

  • Yeremiya 24:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Ndidzachititsa kuti anthu a mitundu yonse padziko lapansi achite mantha akadzaona tsoka limene ndidzawabweretsere.+ Anthu adzawanyoza, adzawaona kuti ndi chitsanzo cha anthu amene akumana ndi tsoka, adzawaseka komanso kuwatemberera+ kulikonse kumene ndidzawabalalitsire.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena