Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 54:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Usachite mantha,+ chifukwa sudzachititsidwa manyazi.+

      Usachite manyazi, chifukwa sudzakhumudwitsidwa.

      Iwe udzaiwala manyazi apaubwana wako,

      Ndipo sudzakumbukiranso kunyozeka kwa paumasiye wako.

  • Yesaya 60:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Ana a anthu amene ankakupondereza adzabwera nʼkudzagwada pamaso pako.

      Anthu onse amene ankakuchitira zachipongwe adzagwada pamapazi ako,

      Ndipo adzakutchula kuti mzinda wa Yehova,

      Ziyoni wa Woyera wa Isiraeli.+

  • Mika 7:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  8 Iwe mdani* wanga, usasangalale chifukwa cha zimene zandichitikira.

      Ngakhale kuti ndagwa, ndidzadzuka.

      Ngakhale kuti ndili mumdima, Yehova adzakhala kuwala kwanga.

  • Zefaniya 2:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  8 “Ndamva kunyoza kwa Mowabu+ ndi mawu achipongwe a Aamoni,+

      Amene ankanenera anthu anga nʼkumadzitama kuti alanda dziko lawo.”+

  • Zefaniya 3:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Pa nthawiyo ndidzalanga onse amene akukupondereza,+

      Ndipo ndidzapulumutsa wotsimphina.+

      Ndidzasonkhanitsa anthu amene anabalalitsidwa.+

      Ndidzachititsa kuti akhale otchuka* komanso azitamandidwa,

      Mʼdziko lonse limene anachititsidwa manyazi.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena