-
Ezekieli 29:3, 4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Umuuze kuti: ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti:
“Ine ndikulanga iwe Farao mfumu ya Iguputo,+
Iwe chilombo chachikulu chamʼnyanja chimene chagona mʼngalande zotuluka mumtsinje wake wa Nailo,+
Ndipo wanena kuti, ‘Mtsinje wa Nailo ndi wanga.
Ineyo ndinaupanga ndekha.’+
4 Koma ine ndidzakukola ndi ngowe munsagwada zako nʼkuchititsa kuti nsomba zamʼngalande za mtsinje wa Nailo zikakamire kumamba ako.
Ndidzakutulutsa mumtsinje wako wa Nailo pamodzi ndi nsomba zonse zamumtsinje wa Nailo zimene zakakamira kumamba ako.
-