-
Ekisodo 20:8-10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Muzikumbukira tsiku la Sabata ndipo muziliona kuti ndi lopatulika.+ 9 Muzigwira ntchito zanu zonse kwa masiku 6.+ 10 Koma tsiku la 7 ndi sabata la Yehova Mulungu wanu. Musamagwire ntchito iliyonse inuyo kapena mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, kapolo wanu wamwamuna, kapolo wanu wamkazi, chiweto chanu kapena mlendo amene akukhala mumzinda wanu.*+
-
-
Levitiko 25:4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Koma mʼchaka cha 7 dzikolo lizidzasunga sabata lopuma pa zonse, sabata la Yehova. Musamadzadzale mbewu mʼminda yanu kapena kudulira mitengo yanu ya mpesa.
-