Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mbiri 28:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Nawonso Afilisiti+ anaukira mizinda ya Yuda ya ku Sefela+ ndi ku Negebu nʼkulanda mzinda wa Beti-semesi,+ wa Aijaloni+ ndi wa Gederoti. Analandanso mzinda wa Soko ndi midzi yake yozungulira, Timuna+ ndi midzi yake yozungulira komanso wa Gimizo ndi midzi yake yozungulira, ndipo anayamba kukhala kumeneko.

  • Yesaya 9:11, 12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Yehova adzakweza adani a Rezini kuti alimbane naye

      Ndipo adzachititsa adani a Isiraeli kuti amuukire,

      12 Siriya adzachokera kumʼmawa ndipo Afilisiti adzachokera kumadzulo,*+

      Iwo adzadya Isiraeli ndi pakamwa potsegula.+

      Chifukwa cha zonsezi, mkwiyo wake sunabwerere,

      Koma dzanja lake lidakali lotambasula kuti awalange.+

  • Yesaya 14:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 “Usasangalale iwe Filisitiya, kapena aliyense wokhala mwa iwe

      Chifukwa chakuti ndodo ya amene ankakumenya yathyoka.

      Chifukwa pamuzu wa njoka+ padzatuluka njoka yapoizoni,+

      Ndipo mwana wake adzakhala njoka youluka, yaululu wamoto.*

  • Yeremiya 47:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 47 Yehova anauza mneneri Yeremiya mawu okhudza Afilisiti,+ Farao asanagonjetse mzinda wa Gaza.

  • Yoweli 3:4-6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Komanso kodi ndakulakwira chiyani

      Iwe Turo ndi Sidoni ndiponso nonse amʼchigawo cha Filisitiya?

      Kodi mukundichitira zimenezi pondibwezera zimene ndinachita?

      Ngati mukundibwezera,

      Ine ndidzakubwezerani mwamsanga ndiponso mofulumira zimene mwandichitirazo.+

       5 Chifukwa chakuti mwatenga siliva ndi golide wanga,+

      Ndipo mwabweretsa zinthu zanga zabwino kwambiri mu akachisi anu,

       6 Komanso mwagulitsa anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kwa Agiriki,+

      Kuti muwapititse kutali ndi dziko lawo,

  • Amosi 1:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  6 Yehova wanena kuti,

      ‘“Chifukwa chakuti Gaza+ wandigalukira mobwerezabwereza, sindidzamusinthira chigamulo changa.

      Chifukwa anatenga anthu onse ogwidwa ukapolo+ nʼkuwapereka ku Edomu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena