-
Ezekieli 25:15, 16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Popeza Afilisiti akupitiriza kuchitira zoipa Aisiraeli chifukwa chodana nawo, iwo akufuna kubwezera komanso kuwononga Aisiraeliwo mwankhanza.*+ 16 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndikutambasula dzanja langa kuti ndilange Afilisiti,+ ndipo ndidzapha Akereti+ nʼkuwononga anthu onse omwe anatsala, amene amakhala mʼmbali mwa nyanja.+
-