-
Ezekieli 27:8, 9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Anthu a ku Sidoni ndi ku Arivadi+ ndi amene ankakupalasa.
Iwe Turo, akatswiri ako odziwa kuyendetsa sitima zapamadzi ndi amene ankakuyendetsa.+
9 Amuna odziwa ntchito* komanso aluso a ku Gebala+ ndi amene ankamata molumikizira matabwa ako.+
Sitima zonse zapanyanja ndi anthu amene ankaziyendetsa ankabwera kwa iwe kudzagulitsa malonda.
-