-
Yeremiya 43:11-13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Nebukadinezara adzabwera nʼkuukira dziko la Iguputo.+ Woyenera kufa ndi mliri adzafa ndi mliri. Woyenera kutengedwa kupita ku ukapolo adzatengedwa kupita ku ukapolo ndipo woyenera kufa ndi lupanga adzafa ndi lupanga.+ 12 Nyumba za milungu* ya ku Iguputo ndidzaziwotcha ndi moto.+ Nebukadinezara adzawotcha nyumbazo nʼkutenga milunguyo kupita nayo kudziko lina. Mʼbusa savutika kuvala chovala chake. Mofanana ndi zimenezi, Nebukadinezara sadzavutika kugonjetsa dziko la Iguputo nʼkuchokako mwamtendere.* 13 Iye adzaphwanyaphwanya zipilala za ku Beti-semesi,* mzinda umene uli ku Iguputo. Ndipo nyumba za milungu* ya ku Iguputo adzaziwotcha ndi moto.”’”
-