-
Ezekieli 28:12, 13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 “Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo yoimba polira yokhudza mfumu ya Turo. Uuze mfumuyo kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti:
13 Iwe unali mu Edeni, munda wa Mulungu.
Unakongoletsedwa ndi miyala yamtengo wapatali yamitundu yonse
Monga rube, topazi, yasipi, kulusolito, onekisi, yade, safiro, nofeki+ ndi emarodi.
Zoikamo miyala imeneyi zinali zagolide.
Ndinazipanga pa tsiku limene ndinakulenga.
-