-
Luka 18:34Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
34 Koma iwo sanamvetse tanthauzo la chilichonse cha zimenezi chifukwa mawu amenewa anabisika kwa iwo ndipo sanamvetse zimene zinanenedwazo.
-
-
1 Petulo 1:10, 11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Aneneri amene analosera za kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu anakusonyezani, anafufuza za chipulumutso chimenechi mwakhama ndiponso mosamala kwambiri.+ 11 Mzimu woyera unali utaneneratu kuti Khristu+ adzavutika ndipo kenako adzalandira ulemerero. Aneneri ankafufuza zizindikiro zimene mzimu woyera* unawasonyeza zokhudza nthawi yeniyeni komanso nyengo imene zimenezi zidzachitike.+
-