Mateyu 24:29 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 29 Chisautso cha masiku amenewo chikadzangotha, dzuwa lidzachita mdima+ ndipo mwezi sudzapereka kuwala kwake. Nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba ndipo mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka.+ Maliko 13:24, 25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 24 Koma mʼmasiku amenewo, chisautso chimenecho chikadzangotha, dzuwa lidzachita mdima ndipo mwezi sudzapereka kuwala kwake.+ 25 Nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba ndipo mphamvu zimene zili kumwamba zidzagwedezeka. Luka 21:25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 Komanso padzakhala zizindikiro padzuwa, mwezi ndi nyenyezi.+ Padziko lapansi anthu a mitundu ina adzazunzika chifukwa chothedwa nzeru poona kuti nyanja ikuchita mkokomo komanso kuwinduka. Chivumbulutso 6:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Atamatula chidindo cha 6, ndinaona kuti kunachitika chivomerezi chachikulu. Dzuwa linada ngati chiguduli choluka ndi ubweya* ndipo mwezi wonse unafiira ngati magazi.+
29 Chisautso cha masiku amenewo chikadzangotha, dzuwa lidzachita mdima+ ndipo mwezi sudzapereka kuwala kwake. Nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba ndipo mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka.+
24 Koma mʼmasiku amenewo, chisautso chimenecho chikadzangotha, dzuwa lidzachita mdima ndipo mwezi sudzapereka kuwala kwake.+ 25 Nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba ndipo mphamvu zimene zili kumwamba zidzagwedezeka.
25 Komanso padzakhala zizindikiro padzuwa, mwezi ndi nyenyezi.+ Padziko lapansi anthu a mitundu ina adzazunzika chifukwa chothedwa nzeru poona kuti nyanja ikuchita mkokomo komanso kuwinduka.
12 Atamatula chidindo cha 6, ndinaona kuti kunachitika chivomerezi chachikulu. Dzuwa linada ngati chiguduli choluka ndi ubweya* ndipo mwezi wonse unafiira ngati magazi.+