48 Potsirizira pake ananyamuka kumapiri a Abarimu nʼkukamanga msasa ku Yeriko, pafupi ndi mtsinje wa Yorodano, mʼchipululu cha Mowabu.+ 49 Anapitiriza kukhala mumsasa pafupi ndi Yorodano, kuyambira ku Beti-yesimoti mpaka ku Abele-sitimu,+ mʼchipululu cha Mowabu.