-
Yesaya 66:20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Adzabweretsa abale anu onse kuchokera ku mitundu yonse+ ngati mphatso kwa Yehova. Adzawabweretsa atakwera mahatchi, ngolo, ngolo zotseka pamwamba, nyulu* ndi ngamila zothamanga, mpaka kukafika kuphiri langa loyera, ku Yerusalemu. Adzachita zimenezi ngati mmene Aisiraeli amabweretsera mphatso mʼnyumba ya Yehova, ataiika mʼchiwiya choyera,” akutero Yehova.
-
-
Yeremiya 31:23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: “Ndikadzasonkhanitsa anthu a mtundu wawo amene anagwidwa nʼkutengedwa kupita kudziko lina, iwo adzanenanso mawu awa mʼdziko la Yuda ndi mʼmizinda yake kuti, ‘Yehova akudalitse iwe malo olungama okhalamo,+ iwe phiri lopatulika.’+
-