23 Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: “Ndikadzasonkhanitsa anthu a mtundu wawo amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina, iwo adzanena mawu awa m’dziko la Yuda ndi m’mizinda yake kuti, ‘Yehova akudalitse iwe+ malo olungama okhalamo,+ iwe phiri lopatulika.’+