Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 22:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Anthu onse ochokera kumalekezero a dziko lapansi adzakumbukira Yehova nʼkupita kwa iye.

      Ndipo mabanja onse a mitundu ya anthu adzagwada pamaso panu.+

  • Yesaya 2:2, 3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  2 Mʼmasiku otsiriza,

      Phiri la nyumba ya Yehova

      Lidzakhazikika pamwamba penipeni pa mapiri akuluakulu,+

      Ndipo lidzakwezedwa kupitirira mapiri angʼonoangʼono.

      Anthu a mitundu yonse adzapita kumeneko.+

       3 Anthu ochokera mʼmitundu yosiyanasiyana adzabwera nʼkunena kuti:

      “Bwerani. Tiyeni tipite kukakwera phiri la Yehova,

      Tipite kunyumba ya Mulungu wa Yakobo.+

      Iye akatiphunzitsa njira zake,

      Ndipo ife tidzayenda mʼnjira zakezo.”+

      Chifukwa chilamulo chidzaphunzitsidwa* mu Ziyoni,

      Ndipo mawu a Yehova adzaphunzitsidwa mu Yerusalemu.+

  • Yesaya 11:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Pa tsiku limenelo muzu wa Jese+ udzaimirira ngati chizindikiro kwa anthu.+

      Anthu a mitundu ina adzatembenukira kwa iye kuti awapatse malangizo,*+

      Ndipo malo ake okhalapo adzakhala aulemerero.

  • Yesaya 55:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 Iwe udzaitana mtundu umene sukuudziwa,

      Ndipo anthu a mtundu umene sukukudziwa adzathamangira kwa iwe

      Chifukwa cha Yehova Mulungu wako,+ Woyera wa Isiraeli,

      Komanso chifukwa chakuti adzakupatsa ulemerero.+

  • Yesaya 60:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  3 Mitundu ya anthu idzatsata kuwala kwako,+

      Ndipo mafumu+ adzatsata ulemerero wako wonyezimira.*+

  • Hoseya 1:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Ndipo Aisiraeli* adzachuluka ngati mchenga wakunyanja umene munthu sangathe kuuyeza kapena kuuwerenga.+ Ndipo kumene ankauzidwa kuti, ‘Siinu anthu anga,’+ adzauzidwa kuti, ‘Ndinu ana a Mulungu wamoyo.’+

  • Mika 4:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  2 Anthu ochokera mʼmitundu yosiyanasiyana adzabwera nʼkunena kuti:

      “Bwerani, tiyeni tipite kuphiri la Yehova,

      Tipite kunyumba ya Mulungu wa Yakobo.+

      Iye akatiphunzitsa njira zake,

      Ndipo ife tidzayenda mʼnjira zakezo.”

      Chifukwa chilamulo,* chidzaphunzitsidwa mu Ziyoni

      Ndipo mawu a Yehova adzaphunzitsidwa mu Yerusalemu.

  • Hagai 2:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 ‘Ndigwedeza mitundu yonse ya anthu, ndipo zinthu zamtengo wapatali zochokera ku mitundu yonse ya anthu zidzalowa mʼnyumba imeneyi.+ Ndipo ndidzadzaza nyumbayi ndi ulemerero,’+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena