2 Mayina a atumwi 12 ndi awa:+ Simoni, amene ankatchulidwa kuti Petulo*+ ndi Andireya+ mchimwene wake. Yakobo mwana wa Zebedayo ndi mchimwene wake Yohane.+
55 Komanso azimayi ambiri ochokera ku Galileya amene ankatsatira Yesu kuti azimutumikira, anali komweko nʼkumaonerera chapatali.+56 Ena mwa iwo anali Mariya wa ku Magadala, Mariya mayi a Yakobo ndi Yose, ndiponso panali mayi a Yakobo ndi Yohane.*+
35 Ndiyeno Yakobo ndi Yohane, ana aamuna a Zebedayo,+ anapita kwa iye nʼkumuuza kuti: “Mphunzitsi, tikufuna kuti mutichitire chilichonse chimene tingakupempheni.”+
2 Simoni Petulo, Tomasi (amene ankatchulidwa kuti Didimo),+ Natanayeli+ wa ku Kana wa ku Galileya, ana a Zebedayo+ ndi ophunzira ake ena awiri onsewa anali pamodzi.