Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Maliko 5:25-34
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Tsopano panali mayi wina amene ankadwala matenda otaya magazi+ kwa zaka 12.+ 26 Madokotala ambiri anamuchititsa kuti avutike kwambiri.* Iye anawononga chuma chake chonse koma sanachire, mʼmalomwake matendawo ankangokulirakulira. 27 Atamva zokhudza Yesu, anakalowa mʼgulu la anthulo nʼkumudzera kumbuyo kwake, kenako anagwira malaya ake akunja.+ 28 Anachita zimenezi chifukwa mumtima mwake ankanena kuti: “Ndikangogwira malaya ake akunja okhawo, ndichira ndithu.”+ 29 Nthawi yomweyo anasiya kutaya magazi ndipo mʼthupi mwake anamva kuti wachira matenda ake aakuluwo.

      30 Nthawi yomweyo, Yesu anazindikira kuti mphamvu+ yatuluka mʼthupi mwake ndipo anatembenuka mʼgulu la anthulo nʼkufunsa kuti: “Ndi ndani wagwira malaya anga akunjawa?”+ 31 Koma ophunzira ake anamuuza kuti: “Inunso mukuona kuti anthu onsewa akukupanikizani, ndiye mungafunse bwanji kuti, ‘Ndi ndani wandigwira?’” 32 Komabe iye ankayangʼanayangʼana kuti aone amene wachita zimenezi. 33 Mayi uja anachita mantha nʼkuyamba kunjenjemera atadziwa zimene zamuchitikira ndipo anafika pafupi nʼkugwada pamaso pake nʼkumuuza zoona zonse. 34 Iye anauza mayiyo kuti: “Mwanawe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere+ ndipo matenda ako aakuluwo atheretu.”+

  • Maliko 6:56
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 56 Ndipo akangolowa mʼmidzi kapena mʼmizinda komanso mʼmadera ozungulira, anthu ankakhazika odwala mʼmisika. Iwo ankamuchonderera kuti angogwira ulusi wopota wamʼmphepete mwa malaya ake akunja,+ ndipo anthu onse amene anaugwira anachira.

  • Luka 8:43-48
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 43 Ndiyeno panali mayi wina amene ankadwala matenda otaya magazi+ kwa zaka 12, ndipo palibe aliyense amene anatha kumuchiritsa.+ 44 Mayiyu anatsatira Yesu kumbuyo nʼkugwira ulusi wopota wamʼmphepete mwa malaya ake akunja.+ Nthawi yomweyo magazi ake anasiya kutuluka. 45 Ndiyeno Yesu anafunsa kuti: “Ndi ndani amene wandigwira?” Onse atakana, Petulo anati: “Mlangizi, simukuona kuti anthu onsewa akuzungulirani ndipo akukupanikizani?”+ 46 Koma Yesu anati: “Ndithu wina wandigwira, chifukwa ndamva mphamvu+ ikutuluka mwa ine.” 47 Mayiyo ataona kuti zimene wachitazo zadziwika, anapita kwa Yesu akunjenjemera ndipo anagwada nʼkuulula pamaso pa anthu onse chimene chinamuchititsa kuti amugwire, komanso mmene wachirira nthawi yomweyo. 48 Koma iye anauza mayiyo kuti: “Mwanawe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena