-
Mateyu 9:20-22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Ndiyeno mayi wina amene ankadwala matenda otaya magazi kwa zaka 12+ anafika kumbuyo kwake nʼkugwira ulusi wopota wamʼmphepete mwa malaya ake akunja,+ 21 chifukwa mumtima mwake ankanena kuti: “Ndikangogwira malaya ake akunja okhawo, ndichira ndithu.” 22 Yesu anatembenuka ndipo anaona mayiyo nʼkunena kuti: “Mwanawe, limba mtima, chikhulupiriro chako chakuchiritsa.”+ Kuchokera pa ola limenelo mayiyo anachira.+
-
-
Maliko 5:25-29Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Tsopano panali mayi wina amene ankadwala matenda otaya magazi+ kwa zaka 12.+ 26 Madokotala ambiri anamuchititsa kuti avutike kwambiri.* Iye anawononga chuma chake chonse koma sanachire, mʼmalomwake matendawo ankangokulirakulira. 27 Atamva zokhudza Yesu, anakalowa mʼgulu la anthulo nʼkumudzera kumbuyo kwake, kenako anagwira malaya ake akunja.+ 28 Anachita zimenezi chifukwa mumtima mwake ankanena kuti: “Ndikangogwira malaya ake akunja okhawo, ndichira ndithu.”+ 29 Nthawi yomweyo anasiya kutaya magazi ndipo mʼthupi mwake anamva kuti wachira matenda ake aakuluwo.
-