-
Luka 11:31, 32Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
31 Mfumukazi yakumʼmwera+ adzaiukitsa kwa akufa pa Tsiku la Chiweruzo limodzi ndi anthu a mʼbadwo uwu ndipo idzawatsutsa, chifukwa mfumukazi imeneyi inabwera kuchokera kumalekezero a dziko lapansi kudzamva nzeru za Solomo. Koma tsopano wina woposa Solomo ali pano.+ 32 Anthu a ku Nineve adzauka pa Tsiku la Chiweruzo limodzi ndi mʼbadwo uwu ndipo adzautsutsa, chifukwa iwo analapa atamva ulaliki wa Yona.+ Koma tsopano wina woposa Yona ali pano.
-