-
Luka 19:20-23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Koma kunabwera wina ndipo ananena kuti, ‘Mbuyanga, ndalama yanu ya mina ija ndi iyi. Ndinaimanga pansalu nʼkuibisa. 21 Ndinachita zimenezi chifukwa ndimakuopani. Inutu ndinu munthu wouma mtima. Mumatenga zimene simunasungitse ndipo mumakolola zimene simunafese.’+ 22 Iye anamuuza kuti, ‘Ndikuweruza potengera zimene wanena, kapolo woipa iwe. Ukuti umadziwa kuti ine ndine munthu wouma mtima, wotenga zimene sindinasungitse ndi kukolola zimene sindinafese.+ 23 Ndiye nʼchifukwa chiyani sunasungitse ndalama yangayo* kubanki? Ukanatero, ine pobwera ndikanaitenga limodzi ndi chiwongoladzanja chake.’
-